Pemphero
Abale Wodala Gerard mu Chichewa / Nyanga
-
Ambuye Yesu
Khristu,
-
Kupyolera
muchaulere chanu mwandiyitana ine kuti ndikutumikireni monga mmodzi mwa
otsatira uBrother wa Gerard Wodalitsika.
-
Ndikukuyamikani pondidalira kuti nditha kugwila ntchitoyi.
-
Ndikukupemphani modzichepetsa, kudzela mwa mayi athu Maria, Yohane
Mbatizi, wodalitsika Gerard Tonque ndi oyera onse kuti mnjira yamoyo
wauzimu wa uBrother uwonekere m’moyo mwanga ndi mnjira zamachitidwe anga
zikhale zodzipereka kuntchito yanu mubanja lathu, kwa anzanga ndi ena
onse ofuna chithandizo changa.
-
Pokhulupilira chithandizo chanu ndikufuna kuti nthawi zonse ndidziteteza
chipembedzo chathu, ndikukhala okonzeka nthawi zonse kuthandiza osowa
kwenikweni osauka, okwiya, aliokha, opunduka and odwala.
-
Ndikukupemphani kuti mundipatse mphamvu zoti ndikwanilitse kusunga
malonjezowa monga mKhristu wamphamvu motsatila chipangano chanu.
-
Mwaulemu wa
Mulungu, mwa mtendere wa dziko lapansi ndi zabwino za anthu onse.
-
Amen.
We thank our member Dr. Chance Chagunda for this translation into
chiChewa / chiNyanja.
Back to the homepage of the Brotherhood of Blessed
Gérard
This page was last updated on
Dienstag, 30 Juni 2020 12:05:18